Child Help Ipempha Boma kuti Lidziwitse Anthu Za Spina Bifida Ndi Hydrocephalus

Bungwe la Child Help lapempha boma ndi mabungwe osiyanasiyana kuti alimbikitse ntchito yodziwitsa anthu za matenda a Spina Bifida ndi Hydrocephalus.

Matendawa amakhudza msana ndi ubongo wa munthu kuyambira pa kubadwa. 

Bungweli lapereka pempholi pamene likukumbukira tsiku la matendawa lero pa 22 October 2026, pansi pa mutu woti, ‘United for SBH: Awareness, Partnership and Resources for Change,’ kutanthauza kugwirizana polimbikitsa chidziwitso, mgwirizano ndi kupeza zipangizo zothandizira anthu omwe ali ndi matendawa.

Poyankhula pamwambowu, mkulu wa bungwe la Child Help, Blessings Chapweteka, wati dziko la Malawi silikuchita bwino pa nkhani yothandiza anthu omwe ali ndi matendawa.

iwo ati kafukufuku akusonyeza kuti anthu pafupifupi 20,000 ali ndi vutoli, pamene anthu pafupifupi 4,000 okha ndi omwe amalandira chithandizo m’zipatala. 

A Chapweteka apemphanso amayi oyembekezera kuti adzipita kuchipatala kuti akhalandire thandizo la uchembere wabwino.

Iwo alimbikitsanso ogwira ntchito m’zipatala kuti adzitumiza msanga mzipatala zikuluzikulu, odwala omwe akuoneka kuti ali ndi zizindikiro za matendawa, kuti akalandire thandizo choyenera.

M’mawu ake, mfumu ya m’zinda wa Blantyre, Isaac Jomo Osman, wati makolo omwe ali ndi ana a Spina Bifida ndi Hydrocephalus akuyenera kuthandizidwa m’njira zosiyanasiyana, kuphatikizapo kuwapezera mwayi wopeza ngongole za boma, chifukwa amakumana ndi mavuto azachuma posamalira ana awo. 

M’modzi mwa makolo, Rachel Dinga wa zaka 30, omwe amakhala ku Monkey Bay m’boma la Mangochi, wati anazindikira za matenda a mwana wake atangobereka kumene, ndipo wapempha anthu ofuna kuthandiza kuti awathandize ndi chakudya, ndalama zoyambira bizinesi ndi zosowa zina.

Mwambowu unasonkhanitsa mabungwe osiyanasiyana, anthu omwe ali ndi Spina Bifida ndi Hydrocephalus, makolo awo komanso anthu ena, ndi cholinga cholimbikitsa mgwirizano komanso kupeza njira zothandizira anthu omwe akukhudzidwa ndi matendawa.

Mirriam Bwanali – Staff Reporter, Blantyre