Chipatala cha Queen Elizabeth Central (QECH) chakhazikitsa ndondomeko yolipiritsa ophunzira omwe amaphunzira ntchito pachipatalachi, ngati njira yofuna kupeza ndalama zobwenzeretsera zipangizo zomwe ophunzirawa amaononga pa nthawi ya ntchito.
Mkulu wa pachipatalachi, Dr. Patrick Dongosolo Kamalo, wauza TVI kuti chipatala cha QECH chiri ndi ntchito zingapo, kuphatikizapo chisamaliro cha odwala komanso kuphunzitsa ophunzira ochokera msukulu zaukachenjede zosiyanasiyana omwe amaphunzitsa zaumoyo mziko muno.
Iwo atinso chipatalachi chaganiza zoyambitsa kulipiritsa ophunzirawa chifukwa choti amaononga zipangizo zochuluka monga magulovu, Mask ndi zina kusiyana ndi ogwira ntchito pachipatalachi.
Dr Kamalo atinso sukulu zomwe zidzitumiza ophunzira awo pachipatalachi ndizomwe zidzilipira ndalamazi zomwe ndi kuyambira K2,000 Kwacha mpaka K20,000 sabata iriyonse.
Malingana ndi ndondomeko yatsopanoyi, ophunzira omwe amaphunzira kunja kwa dziko lino adzilipira K20,000 pa sabata pomwe ophunzira a mdziko muno adzilipira K2,000 pa sabata.
Wolemba: Mirriam Bwanali, Blantyre

