“Ogwira Ntchito Adzitetezeka Pa Ntchito,” yatero MEHA.

Bungwe la Malawi Environmental Health Association (MEHA) lalangiza olemba ntchito mdziko muno kuti awonetsetse kuti malo awo ogwilira ntchito akuthandizira kupititsa patsogolo umoyo wa ogwira ntchito powateteza ku ngozi komanso matenda osiyanasiyana.

‎Mtsogoleri wa bungwe la MEHA, Bertha Sato, walankhula izi Lachisanu, pamene dziko lonse likukumbukira tsiku loona za chitetezo ndi umoyo wabwino m’malo ogwira ntchito, lomwe mwambo wokumbukira umakhala pa 28 April chaka chirichonse.

‎Polankhula ndi TVI, a Sato atsindika kuti olemba ntchito ndi ogwira ntchito ali ndi udindo uwonetsetsa kuti malo awo ogwirira ntchito sakuika chiopsezo pa umoyo wa anthu polingalira kuti anthu ochuluka amakhala nthawi yaitali m’malo ogwirira ntchito osiyanasiyana.

‎A Sato atinso pambali pothandizira ogwira ntchito ndi zipangizo zowatetezera ku ngozi komanso matenda osiyanasiyana, olemba ntchito akuyenera kuonetsetsa kuti malo awo ogwirira ntchito akuthandizira kulimbikitsa malingaliro a m’ngwiro kwa ogwira ntchito popewa kuwachitira nkhanza zosiyanasiyana ogwira ntchito.

Mutu wa chaka chino ndi woti, “Kulimbikitsa Umoyo Wabwino Wa M’malingaliro M’malo Ogwilira Ntchito.

‎(Wolemba: Edward Rex)