IIB Yayamba Kuphunzitsa Ma Sheikh Ndi Ma Imam Za Utsogoleri Wabwino

Bungwe la Islamic Information Bureau (IIB) layamba kupereka maphunziro okhudza utsogoleri wabwino kwa ma Sheikh ndi ma Imam ochokera m’madera osiyanasiyana a dziko lino.

Malinga ndi woyendetsa ntchito ku Limbe Islamic Information Bureau, Sheikh Khalifah Idruss, izi zikuchitika pofuna kuwalimbikitsa kuti azitsogolera bwino anthu omwe ali pansi pa utsogoleri wawo.

Sheikh Idruss ati maphunzirowa akuyembekezeka kutenga miyezi isanu ndi inayi, kuyambira mwezi wa October chaka chino mpaka mwezi wa June chaka chamawa.

Iwo ati maphunzirowa adzichitika kawiri pamwezi ndipo cholinga chake ndi kupititsa patsogolo luso la ma Sheikh ndi ma Imam pa nkhani za utsogoleri, makamaka pa momwe angatsogolere anthu m’mizikiti komanso m’madera omwe amagwirira ntchito.

Sheikh Idruss ati maphunzirowa athandizanso atsogoleri achipembedzo kukhala ndi luso lopanga zisankho zoyenera pa nkhani zosiyanasiyana zokhudza chipembedzo.

Maphunzirowa akupereka ndi ma Sheikh anayi ochokera ku Limbe Islamic Information Bureau ndi ma Sheikh atatu ochokera ku Majlis Ulama Council of Malawi.

Edward Rex – Staff Reporter, Blantyre