Nduna yoona za Ulimi ndi Chitukuko cha Madzi, Roza Mbilizi, yayendera malo omwe bungwe la Southern Region Water Board komanso Blantyre Water Board limatenga madzi ku Likhubula m’boma la Mulanje.
A Mbilizi achita izi pofuna kudziwa zomwe zikuchititsa vuto la kusowa kwa madzi komanso kupeza njira zothetsera vutoli.
Paulendowu, ndunayi yayendera malo osiyanasiyana omwe amagwiritsidwa ntchito potungira ndi kupereka madzi, kuti imvetsetse momwe ntchito yopezera madzi imayendera.
A Mbilizi ati ulendowu ndi gawo limodzi la khama la boma lofuna kuzindikira zomwe zikulepheretsa anthu kupeza madzi okwanira komanso abwino, ndi kupeza njira zokhazikika zothetsera vutoli.
Ndunayi yatsindikanso kufunika kogwirizana pakati pa boma ndi mabungwe omwe amapereka madzi pofuna kuonetsetsa kuti anthu akupeza madzi mosavuta komanso mosalekeza.
Paulendowu panalinso mkulu wa bungwe la Southern Region Water Board, Gladys Ganda ndi Bwanamkubwa wa boma la Mulanje, Chriss Nawata.
Ulendowu ukubwera pomwe anthu akufunika njira zokhazikika zothetsera mavuto a madzi, zomwe zikupangitsa kuti pakhale kufunika kowunika momwe madzi amatungidwira, kusungidwira komanso kufikitsidwira kwa anthu.
Myson Julius Saidi – Staff Reporter, Blantyre

