MEDF Yayambiranso Kupereka Ngongole

Bungwe la Malawi Enterprise Development Fund (MEDF) layambiranso kupereka ngongole m’chaka cha boma cha 2026/27, pomwe laika pambali ndalama zokwana K100 biliyoni zothandizira anthu kuchita malonda osiyanasiyana m’dziko muno.

Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe, Mkulu wa MEDF, Kaisi M’bwana Sadala, wati bungweli lachepetsa mitundu ya ngongole kuchokera pa 26 kufika pa magulu asanu ndi anayi (9) pofuna kupititsa patsogolo kayendetsedwe ka ntchito komanso kuti anthu adzitha kupeza ngongole mosavuta.

Ena mwa magulu a ngongole zomwe zikuperekedwa ndi ngongole zothandizira achinyamata, amayi, abambo komanso ngongole za chitukuko cha ulimi, pamodzi ndi magulu ena osiyanasiyana.

A M’bwana Sadala atinso MEDF ikulimbikitsa anthu ofuna kubwereka kuti adzikhala m’magulu a anthu osachepera khumi (10).

Malinga ndi a M’bwana sadala, izi zikuchitika pofuna kuchepetsa vuto la kulephera kubweza ngongole.

Panthawiyi, MEDF yaululanso kuti anthu opitilira theka omwe analandira ngongole m’magawo am’mbuyomu sanabwenze ngongole zawo, ndipo bungweli lati chiwerengerochi ndi chokwera kwambiri poyerekeza ndi momwe mabanki amalonda ndi mabungwe ena obwereketsa ndalama amapezera ndalama zawo kuchokera kwa obwereka.

(Wolemba, Aspolo Mousah, Lilongwe