Gulu la Concerned Citizens of Malawi-People Power Movement Lalepheletsa Zionetsero

Gulu la Concerned Citizens of Malawi-People Power Movement lalepheletsa zionetsero zimene linakomza Lachiwiri pa 17 November, 2026.
Wapampando wa gululi, Edwards Kambanje, watsimikiza izi pa msokhano wa atolankhani ku Blantyre.
Gululi linalengeza masiku apitawo kuti lichita zionetsero m'maboma a Blantyre, Zomba, Mzuzu ndi Lilongwe, poonetsa mkwiyo ndikusayenda kwa zinthu.
Mlembi wa mkulu wagululi, Prince Mattaka, anatsindikanso mu pologalamu ya Pambalambanda pa TVI kuti palibe kusintha kulikonse, ngakhale zokambirana zinali kupitilira kuchitika ndi adindo pofuna kupeza mayankho ku mavuto a kuzimazima kwa magetsi, kusowa kwa mafuta ndi kusowa kwa ndalama zakunja.
Koma poyankhula ndi atolankhani, a Kambanje ati aimitsa zionetserozi pofuna kupereka mpata ku zokambirana ndi unduna wa zamagetsi komanso bungwe la ESCOM omwe atsimikiza kuti vutoli likomzedwa msanga.
Pakadalipano, gululi lachenjeza mabungwe ndi magulu a anthu omwe anakonza zipolowe pazionetserozi kuti asagwilitse ntchito dzina la Concerned Citizens - People Power Movement.
Komabe a Kambanje ati ngati mavutowa sakomzedwa, gulu lawo lidzakonzanso zionetsero pofuna kuti adindo asamangoyang'anira nzika za dziko lino zikuzumzika.


