Katswiri pa nkhani za chuma, Christopher Mbukwa, wati kutsika kwa mtengo wa mafuta a Petrol kuthandiza kukhazikika kwa mitengo ya katundu yomwe yakhala ikukwera.
Poyankhula ndi TVI, a Mbukwa ati kutsika kwa mtengo wa mafuta ndi chimodzi mwa zipatso zabwino za ndondomeko ya Automatic Fuel Pricing Mechanism.
Iwo ati ndi ndondomekoyi, anthu ambiri amayembekezera kuti mafuta apitiriza kukwera mtengo chifukwa cha nkhondo yomwe ilipo pakati pa America-Israel ndi Iran.
Komabe, a Mbukwa ati ngakhale mafuta a Petrol atsika mtengo pang’ono, katundu wambiri akhalabe pa mitengo yokwera chifukwa mtengo wa mafuta a Diesel sunatsike.
A Mbukwa ati mitengo ya katundu itsika ngati mtengo wa mafuta a Diesel ungatsike.
Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) latulutsa chikalata chotsitsa mtengo wa mafuta a Petrol kuchoka pa K6,672 kufika pa K6,209 pa lita imodzi, zomwe zikutanthauza kuti atsika ndi K6.94 pa K100 iliyonse.

